۞ يَسْـَٔلُوْنَكَ عَنِ الْخَمْرِ وَالْمَيْسِرِۗ قُلْ فِيْهِمَآ اِثْمٌ كَبِيْرٌ وَّمَنَافِعُ لِلنَّاسِۖ وَاِثْمُهُمَآ اَكْبَرُ مِنْ نَّفْعِهِمَاۗ وَيَسْـَٔلُوْنَكَ مَاذَا يُنْفِقُوْنَ ەۗ قُلِ الْعَفْوَۗ كَذٰلِكَ يُبَيِّنُ اللّٰهُ لَكُمُ الْاٰيٰتِ لَعَلَّكُمْ تَتَفَكَّرُوْنَۙ
yas'alūnaka ‘anil-khamri wal-maisir(i), qul fīhimā iṡmun kabīrw wa manāfi‘u lin nās(i), wa iṡmuhumā akbaru min naf‘ihimā, wa yas'alūnaka māżā yunfiqūn(a), qulil-‘afw(a), każālika yubayyinullāhu lakumul-āyāti la‘allakum tatafakkarūn(a).
Anakufunsani (Muhammad) za mowa ndi kutchova juga. Nena, "M'zonsezi muli uchimo waukulu ndi ubwino wina kwa anthu. Koma uchimowo ndi waukulu kuposa ubwino." Ndipo akukufunsani (za) zomwe ayenera kupereka. Nenani, "Zowonjezera (pa zomwe zikufunika)." Momwemo Mulungu akukufotokozerani ma vesi Ake kuti muganize,
يٰٓاَيُّهَا الَّذِيْنَ اٰمَنُوْٓا اِنَّمَا الْخَمْرُ وَالْمَيْسِرُ وَالْاَنْصَابُ وَالْاَزْلَامُ رِجْسٌ مِّنْ عَمَلِ الشَّيْطٰنِ فَاجْتَنِبُوْهُ لَعَلَّكُمْ تُفْلِحُوْنَ
yā ayyuhal-lażīna āmanū innamal-khamru wal-maisiru wal-anṣābu wal-azlāmu rijsum min ‘amalisy-syaiṭāni fajtanibūhu la‘allakum tufliḥūn(a).
E inu amene mwakhulupirira! Ndithudi, kumwa mowa, kutchova njuga, kupereka nsembe kwa mafano, ndi kukopa chuma chambiri ndi mivi, ndi zinthu zoipa kwambiri ndipo ndi zina mwa zochita za Satana. Choncho pewani zimenezo kuti mukhale ndi mwayi.
وَلَا تَقْرَبُوا الزِّنٰىٓ اِنَّهٗ كَانَ فَاحِشَةً ۗوَسَاۤءَ سَبِيْلًا
wa lā taqrabuz-zinā innahū kāna fāḥisyah(tan), wa sā'a sabīlā(n).
Ndipo musayandikire chigololo, ndithudi, ndi chinthu chonyansa komanso njira yoipa.