223
Q.S Al-Baqarah (2:223)
نِسَاۤؤُكُمْ حَرْثٌ لَّكُمْ ۖ فَأْتُوْا حَرْثَكُمْ اَنّٰى شِئْتُمْ ۖ وَقَدِّمُوْا لِاَنْفُسِكُمْ ۗ وَاتَّقُوا اللّٰهَ وَاعْلَمُوْٓا اَنَّكُمْ مُّلٰقُوْهُ ۗ وَبَشِّرِ الْمُؤْمِنِيْنَ
nisā'ukum ḥarṡul lakum, fa'tū ḥarṡakum annā syi'tum, wa qaddimū li anfusikum, wattaqullāha wa‘lamū annakum mulāqūh(u), wa basysyiril-mu'minīn(a).
Akazi anu ndi munda wanu, choncho bwerani kumunda wanu nthawi iliyonse komanso momwe mungafunire. Ndipo perekani patsogolo (zabwino) zanu. Opani Mulungu ndipo dziwani kuti (tsiku lina) mudzakumana naye. Ndipo lengezani nkhani yabwino kwa okhulupirira.